Jump to content

Afilika

From Wikipedia
(Redirected from Africa)
Afilika
Afilika

Afilika ndi chigawo chimodzi cha zigawo za pa dziko la pansi ndipo ndi chigawo cha chiwiri kwa madela lomwe kuli anthu ambiri, koma anthu ambiri ali ku Asia. Ku Africa kumakhala 14% ya anthu onse a pa dziko la pansi, chifukwa chiwelengelo cha anthu ku Afilika ku ndi 1 300 miliyoni ( malinga ndi chiwelengelo cha anthu chomwe chinachitika mu 2013). Gawo la Afilika lili ndi mayiko 53, ndipo linazungulilidwa nsi nyanja ya Mediterranean kumpoto, nyanja ya Red Sea kumpoto chakumvuma, nyanja ya Indian kummwera cha kumvuma ndi nyanja ya Atlantic kuzambwe. Pali mayiko 46 a mu Africa ndi 53 kuphatikiza zilumba zonse.

Afilika, makamaka kumvuma kwa delari, kumatchuka kwambiri kuti ndi kumene anthu anachokera mtundu wa anthu ndipo anapezako zotsalira za anthu amene analipo zaka 7 miliyoni zapitazo.

Dera la Afilika lili mbali zonse ziwiri za mzere wa Equator ndipo nyengo za mudelari zimasiyana siyana kumpoto ndi kummwera kwa mzerewu.

Kumene kunachokela dzinali

[Sinthani | sintha gwero]

Afili linali dzina la anthu amene ankakhala kumpoto kwa dela la Africa ku malo otchedwa Carthage. –Ca, amatanthauza anthu kapena malo. Anthu ena amaganiza kuti dzina loti Afilika linachokela ku: Liu la chilatini lakuti aprica limene limatanthauza malo owala dzuwa kwambiri

Liu la chigiriki aphrike limene limatanthauza malo amene sikumazizira.

Kakhalidwe ka malo ku derali

[Sinthani | sintha gwero]

Dziko lalikulu kwa mbiri kudera la Afilika ndi la Sudan ndipo dziko lake laing‘ono kwambiri ndi la Seychelles lomwe ndi chilumba ku mmawa kwa delari. Dziko laling’ono pa gombe ndi Gambia.

Munthu mozama pa nkhani za kakhalidwe ka dziko a Ptolemy (85-165 AD) ndi amene anagawa Afilika kuchokela ku dera la Asia ndipo anasiya Nyanja yofiira ngati malire. Kulinso munthu wina dzina lake Pearson Mpindi fatch ndi thug.

Nyengo, zachilengedwe ndi zomera

[Sinthani | sintha gwero]

Nyengo ku Afilika imayambira kukhala yotentha komanso yozizira kwambiri. Kumpoto kwa delari ndi kuchipululu ndi kotentha, pamene pakati ndi kummwera ndi kotentha komanso kuli nkhalango zowilira kwambiri. Pali Madela ena amene kuli nyengo zotentha kwambiri komanso zozizira kwambiri.